Vuto la Milatho ku Zolozolo

18-Feb-2020 | 11:27

Zolozolo East ward kuli vuto la milatho moti ana akumavutika kuoloka kuti apite pa Zolozolo primary school

Tiyamike Ntchito Yokonza Mseu

18-Feb-2020 | 11:23

Kuno ku Kasungu msewu womwe unaonongeka ma yenje ayamba kuukonza

Program Yokonza Miseu

17-Feb-2020 | 15:36

Kuno kwathu program yokonza miseu yidaimila panjira monga mseu wa kwa Senya to Chitete river ndi Kapindula to Chitete. Sitikudziwa kuti asembule ma plan awo ndiotani

Security Concern in Mwima

11-Feb-2020 | 08:28

Balaka Shire ward umbava wavuta ku Mwima. Every week kumapezeka shop yabedwa

Ku Masakapande Vuto la Bridge

09-Feb-2020 | 18:27

Ku Masakapende kuli vuto la bridge yomwe inaphotchoka kale kale koma siyikukonzedwa

Funso pa za tsiku lotsegulira Chipatala

07-Feb-2020 | 08:33

Chipatala cha Mwima chatha zaka 17 koma osachitsegulila. Anthu adandaula koma kuli zii

Kusowa Kwa Ma Toilet Abwino M'misika

06-Feb-2020 | 07:44

Kuno ku Kasungu misika yambiri ing'onoing'ono mulibe ma toilet koma ma tiketi timaduladaily. Kodi ndalamazo zimagwira ntchito yanji

Kufunikira kwa Ngalande ku Kasungu

05-Feb-2020 | 10:48

Ngalande za mu msika ndi zosafukula kuno ku Kasungu chinthu chomwe chikupangisa kuti madzi azilowa pamalo ogulitsira malonda

Mutiunikire Za Malata Subsidy

05-Feb-2020 | 08:16

Kasungu West kwa Sub-TA Mawawa, kodi boma bwanji likupereka zithu zochepa pazipangizo zomwe adalonjeza? Ndalama ya labor K50,000 sakutipatsa, ma door frame ndi mawindow sakutipatsa. kodi nanga ngongoleyi tizabweza bwanji ngati katundu wina sititenga

Poor roads

24-Jan-2020 | 08:53

Ine ndimakhala ku zingwangwa ku BT, ndimati ndidandaule miseu yathu mu dela limeneli siili bwino. Maenje maenje ndithu ndiye madzi a mvula akumadikha mmenemu, sizili bwino ndithu

Njala ku Balaka

21-Jan-2020 | 11:14

Njala yafika povuta ku balaka makamaka dela la Mfumu yaikulu Phimbi pomwe anthu anayi sabata yatha anakomoka ndi njala zomwe zapangitsa phungu wa delali Ireen Mambala kugawa chakudya kwa ena mu delali

Poor road

21-Jan-2020 | 07:36

kuno ku nkaya athu akumagwira ntchito za find your feet koma akulephela kulandila chimanga chifukwa ogawa akusowa kuti ayenda bwanji chifukwa cha nsewu. Izi sikupangisa kuti anthu agone ndi njala

Kusatuluka Kwa Madzi

20-Jan-2020 | 21:15

Kusatuluka kwa madzi mmalo ena oyandikira pa town assembly kuno ku Kasungu kukweza chiophyeza chakufala kwa matenda odza Kamba ka Ntchetche

Vuto la nseu

20-Jan-2020 | 08:55

vuto la nseu kuno ku ngerenge karonga. wadyeka kwambiri magalimoto akulephera kudusa

Kusowa Chilungamo pakagawidwe ka Chimanga

14-Jan-2020 | 10:31

Kuno ku Balaka Central East kagawidwe ka chimanga sikakuyenda bwino, ma khansala and akulu akulu azipani kumadera akumangoba thandizolo likabwera

Kuchepa Kwa Chitetezo

11-Jan-2020 | 03:22

Kuno ku Kasungu Chitetezo chachepa anthu akumalanga okha akuba. chonde tithandizeni